Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 5:23 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 “ ‘Wansembe alembe matemberero amenewa mʼbuku ndi kuwanyika mʼmadzi owawa aja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

23 Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 “Wansembe alembe m'buku matemberero ameneŵa ndipo aŵafafanize poŵaviika m'madzi oŵaŵa aja.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:23
14 Mawu Ofanana  

‘Yehova akunena kuti, Ine ndidzabweretsa mavuto pamalo pano ndi pa anthu ake, matemberero onse amene alembedwa mʼbukuli amene awerengedwa pamaso pa mfumu ya Yuda.


“Aa, pakanakhala wina wondimva! Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe; mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.


Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.


Mufulatire machimo anga ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”


“Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini, ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.


Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo, ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa. Bwerera kwa Ine, popeza ndakupulumutsa.”


Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’ ” “Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’ ”


Amwetse mkaziyo madzi owawawo omwe amabweretsa temberero, ndipo madzi amenewo adzalowa mʼmimba mwake ndi kuyambitsa ululu woopsa.


Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,


“Tsopano ulembe mawu a nyimbo iyi ndipo uwaphunzitse Aisraeli, uwawuze kuti aziyimba, kuti ikhale mboni yanga yowatsutsa.


Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa