Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.
Numeri 4:24 - Buku Lopatulika Ntchito ya mabanja a Ageresoni, pogwira ntchito ndi kusenza katundu ndi iyi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ntchito ya mabanja a Ageresoni, pogwira ntchito ndi kusenza katundu ndi iyi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene mabanja a Geresoni ayenera kuchita, ndiponso zimene ayenera kumanyamula ndi izi: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi: |
Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.
Ndipo udikiro wa ana a Geresoni m'chihema, chokomanako ndiwo Kachisi, ndi chihema, chophimba chake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako,
ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.
koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake aamuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.
Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.
azinyamula nsalu zophimba za Kachisi, ndi chihema chokomanako, chophimba chake, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu chili pamwamba pake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako;
Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.
kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira ntchito ya utumikiwu, ndiyo ntchito ya akatundu m'chihema chokomanako;
Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.