Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 4:23 - Buku Lopatulika

23 Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Uwerenge amuna onse a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu zakubadwa amene amabwera kudzatumikira ku tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:23
18 Mawu Ofanana  

Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.


Pakuti monga mwa mau ake otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.


Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.


Werenganso ana a Geresoni, monga mwa nyumba za makolo ao, monga mwa mabanja ao.


Ntchito ya mabanja a Ageresoni, pogwira ntchito ndi kusenza katundu ndi iyi;


kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako.


ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi;


Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?


m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,


Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.


Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.


Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;


Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa