Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 10:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anagwetsa Kachisi; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula Kachisi, anamuka naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Anthu atagwetsa chihema cha Mulungu, ana a Geresoni ndi ana a Merari, oyenera kunyamula chihema cha Mulungu, adanyamuka ulendo wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 10:17
11 Mawu Ofanana  

Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.


Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.


Ndi gulu la fuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.


Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.


Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.


Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,


podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa