Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 4:49 - Buku Lopatulika

49 Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Anthuwo adaŵasankha kuti ena azigwira ntchito yotumikira, ndipo ena azinyamula katundu, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Umu ndimo m'mene adaŵaŵerengera anthuwo, monga momwe Chauta adaamlamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 4:49
18 Mawu Ofanana  

Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo.


Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.


Koma sanawerenge Alevi mwa ana a Israele; monga Yehova adauza Mose.


Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ntchito ya mabanja a Ageresoni, pogwira ntchito ndi kusenza katundu ndi iyi;


Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako ndi ichi: matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake;


ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao.


Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.


Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Geresoni, onse akutumikira m'chihema chokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.


Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa