Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Numeri 34:12 - Buku Lopatulika ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa atsike ndithu mpaka ku mtsinje wa Yordani, ndipo akathere ku Nyanja ya Mchere. Limeneli ndilo dziko lanu pamodzi ndi malire ake ozungulira dzikolo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. “ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ” |
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.
Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.
ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;
dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa;
Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao.
Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;