taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;
Numeri 32:5 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngati mwatikomera mtima, mutipatse dzikoli atumiki anufe, kuti likhale lathu. Musatipititse patsidya pa Yordani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’ ” |
taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;
Ndipo Yowabu anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yowabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yachita chopempha mnyamata wake.
Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.
Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.
dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.
Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?
Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani!
Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.