Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 32:4 - Buku Lopatulika

4 dzikoli Yehova analikantha pamaso pa gulu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 dziko limene Chauta adagonjetsera Aisraele, ndi dziko loyenera kuŵeterako ng'ombe, ndipo atumiki anufe tili ndi ng'ombe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 32:4
9 Mawu Ofanana  

Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.


Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi mu Giliyadi.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.


Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.


Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.


Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani.


kupirikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa