Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo.