Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 20:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma Davide adalumbira kuti, “Abambo ako akudziŵa bwino lomwe kuti umandikonda, ndipo adati, ‘Yonatani asadziŵe zimenezi kuwopa kuti angamve chisoni.’ Koma ndithu, Mulungudi, iwe Yonatani uli apa, imfa sili nane kutali.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma Davide analumbira kuti, “Abambo ako akudziwa bwino lomwe kuti iwe umandikonda ndipo iwo amaganiza kuti, Yonatani sayenera kudziwa zimenezi mwina adzamva chisoni kwambiri. Komabe, pali Yehova ndi pali iwe, imfa sinanditalikire.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 20:3
18 Mawu Ofanana  

Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu.


Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele.


Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.


Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.


Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.


Ndipo mfumu Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu.


Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake.


Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.


Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.


Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.


Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.


Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Chilichonse mtima wako, unena ndidzakuchitira.


Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.


Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa