Yoswa 7:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani! Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani! Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono Yoswa adati, “Kalanga ine Chauta! Chifukwa chiyani mudatiwolotsa Yordani? Kani mudatipereka m'manja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Bwanji osangotileka kuti tikhale tsidya ilo la Yordani? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani! Onani mutuwo |