Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Estere 5:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo.

Onani mutuwo Koperani




Estere 5:2
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.


Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.


Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu.


Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.


Ndimkonda, popeza Yehova amamva mau anga ndi kupemba kwanga.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.


namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa