Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 31:2 - Buku Lopatulika

2 Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mau a Chauta ndi aŵa, “Anthu amene adapulumuka ku nkhondo, ndidaŵakomera mtima m'chipululu. Pamene Aisraele ankafuna kupumula,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova akuti, “Anthu amene anapulumuka ku nkhondo ndinawakomera mtima mʼchipululu; pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 31:2
32 Mawu Ofanana  

Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu.


Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.


ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.


Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.


ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.


Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo.


Ndipo ndidzalowa nanu m'chipululu cha mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso.


Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya.


Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.


Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako:


Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.


Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu;


amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.


pakuti mpaka lero simunafikire mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.


Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.


amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;


Kumbukirani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa