Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;
Numeri 32:22 - Buku Lopatulika ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa mpaka kugonjetsa dzikolo pamaso pa Chauta. Mukatero, pambuyo pake mudzabwerera kuno, chifukwa mudzakhala mutagwirira ntchito Chauta ndi Aisraele. Pamenepo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova. |
Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;
Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.
Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;
ndi kuoloka Yordani pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapirikitsa adani ake pamaso pake,
kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.
mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanulanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordani la kum'mawa,
ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yake m'dzanja la Israele; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namchitira mfumu yake monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.
Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo.
Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale cholowa chao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.
Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;
Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.
Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.
Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.