Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 13:8 - Buku Lopatulika

8 Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndiponso theka lina lija la fuko la Manase adalandira dziko lao cha kuvuma kwa Yordani. Dziko limeneli ndilo lija adaŵapatsa Mose mtumiki wa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 13:8
11 Mawu Ofanana  

Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa.


Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni;


Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa;


Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi hafu la fuko la Manase, likhale cholowa chao.


Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi hafu la fuko la Manase, dziko ili likhale cholowa chao.


kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;


Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;


Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordani nafika ku dziko la Gadi ndi Giliyadi; koma Saulo akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa