Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 22:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Motero anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase, adabwerera kwao. Aisraele ena onse adaŵasiya ku Silo m'dziko la Kanani, ndipo iwowo adapita ku dziko la Giliyadi. Dziko limeneli ndilo linali lao, chifukwa adalilandira potsata malamulo a Chauta kudzera mwa Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Choncho mafuko a Rubeni, Gadi, pamodzi ndi theka la fuko la Manase anabwerera kwawo. Aisraeli ena onse anawasiya ku Silo mʼdziko la Kanaani. Tsono anapita ku dziko la Giliyadi, dziko limene linali lawo popeza analilandira potsata malamulo a Yehova kudzera mwa Mose.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 22:9
19 Mawu Ofanana  

namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.


ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kuchipululu kuyambira mtsinje wa Yufurate; pakuti zoweta zao zinachuluka m'dziko la Giliyadi.


Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.


Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.


Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzachita ichi, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,


ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova.


Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'mizinda ya ku Giliyadi;


Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;


Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.


kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.


Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;


ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka;


Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;


ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.


Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake.


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani; ndi Dani, akhaliranji m'zombo? Asere anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja, nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa