Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 22:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsopano Chauta, Mulungu wanu, wapatsa mtendere Aisraele anzanu, monga momwe adaalonjezera. Motero bwererani kwanu ku dziko limene mudalandira, dziko limene lili patsidya pa mtsinje wa Yordani kuvuma, limene Mose mtumiki wa Chauta adakupatsani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono pakuti Yehova Mulungu wanu wapereka mpumulo kwa abale anu monga anayankhulira nawo, bwererani ku nyumba zanu ku dziko limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, dziko limene lili pa tsidya la Yorodani kummawa.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 22:4
16 Mawu Ofanana  

Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Sanakupumulitseni pambali ponse? Pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ake.


Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.


Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israele atalandira yense cholowa chake.


pakuti mpaka lero simunafikire mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.


ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale cholowa chao cha Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase.


kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.


Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina.


mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanulanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordani la kum'mawa,


Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi hafu la fuko la Manase, likhale cholowa chao.


Ndipo Mose anapatsira fuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao.


Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;


simunasiye abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga chisungire lamulo la Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa