Pakuti monga mwa mau ake otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Numeri 3:8 - Buku Lopatulika Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aziyang'anira zipangizo zonse za m'chihema chamsonkhano, ndipo azigwirira Aisraele ntchito potumikira m'Chihema cha Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Azisamalira zipangizo zonse za mu tenti ya msonkhano, ndipo azigwirira ntchito Aisraeli potumikira mu tenti. |
Pakuti monga mwa mau ake otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.
Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.
Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.
Ndipo azisunga udikiro wake, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la chihema chokomanako, kuchita ntchito ya Kachisi.
Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele.
Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.
Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Geresoni m'chihema chokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao.
Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.