Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Aleviwo uŵapereke kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna. Uŵapereke kwathunthu kwa iyeyo, kuŵachotsa pakati pa Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pereka Alevi kwa Aaroni ndi kwa ana ake aamuna. Amenewa ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwa iye kwathunthu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:9
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.


Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woimbayo, mwana wa Yowele, mwana wa Samuele,


Antchito a m'kachisi: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,


Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.


ndi antchito a m'kachisi, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, antchito a m'kachisi mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo otchulidwa maina.


kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku gulu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya chihema cha Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;


Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni.


Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi.


Momwemo upatule Alevi mwa ana a Israele; kuti Alevi akhale anga.


Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele.


Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele.


Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake aamuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika.


Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;


Chifukwa chake anena, M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa