Numeri 31:30 - Buku Lopatulika30 Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201430 Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa Kachisi wa Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa30 Ndipo pa gawo la Aisraele, mtengeko chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, pa anthu, ng'ombe, abulu, nkhosa ndi pa nyama zonse zoŵeta, ndipo mupatse Alevi amene amayang'anira Chihema cha Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero30 Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.” Onani mutuwo |