Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 31:29 - Buku Lopatulika

29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Mutenge zimenezo pa gawo la ankhondowo ndipo mupatse wansembe Eleazara, kuti zikhale zopereka zanu kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Utenge zimenezo pa theka la gawo la ankhondowo ndipo upereke kwa wansembe Eliezara kuti zikhale zopereka zanu kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 31:29
7 Mawu Ofanana  

Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;


Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israele, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale cholowa chanu chochokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.


Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.


Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.


Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.


Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.


Dzichenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa