Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo azisunga udikiro wake, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la chihema chokomanako, kuchita ntchito ya Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo azisunga udikiro wake, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la chihema chokomanako, kuchita ntchito ya Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Azigwirira ntchito iyeyo ndi mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, monga momwe amachitira potumikira m'Chihema cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Azigwira ntchito yothandiza iyeyo ndi gulu lonse ku tenti ya msonkhano pogwira ntchito ya ku Chihema.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:7
13 Mawu Ofanana  

Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi chuma cha zopatulika.


Ana a Yehiyeli: Zetamu ndi Yowele mbale wake, oyang'anira chuma cha nyumba ya Yehova.


Selomoti amene ndi abale ake anayang'anira chuma chonse cha zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akulu a nyumba za akulu, akulu a zikwi ndi mazana, adazipatula.


Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.


koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pamalo opatulika.


Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi.


Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.


ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova.


Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa