Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
Numeri 3:4 - Buku Lopatulika Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Nadabu ndi Abihu adafa pamaso pa Chauta pamene adapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta m'chipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana, ndipo choncho Eleazara ndi Itamara adatumikira pa ntchito yaunsembe pa nthaŵi imene Aroni bambo wao anali moyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo. |
Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.
ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.