Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma Nadabu ndi Abihu adafa pamaso pa Chauta pamene adapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta m'chipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana, ndipo choncho Eleazara ndi Itamara adatumikira pa ntchito yaunsembe pa nthaŵi imene Aroni bambo wao anali moyo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:4
7 Mawu Ofanana  

Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.


Ndipo moto wochokera kwa Yehova unabwera nʼkunyeketsa anthu 250 amene ankapereka nsembe yofukiza aja.


Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo.


Tenga Aaroni ndi mwana wake wamwamuna Eliezara ndipo ukwere nawo ku phiri la Hori.


Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).


Yehova anati kwa Mose,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa