Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 19:3 - Buku Lopatulika

3 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Muupereke kwa wansembe Eleazara, kenaka anthu atuluke nawo kunja kwa mahema, ndipo auphe pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 19:3
11 Mawu Ofanana  

Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.


Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.


Natulutse chikopa cha ng'ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,


inde ng'ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.


Ndipo atulutse ng'ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.


Pamenepo khamu lonse linamtulutsa kunja kwa chigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.


Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.


Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.


Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa