Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 16:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Tsono padayaka moto wochokera kwa Chauta ndipo udapsereza anthu 250 amene ankafukiza lubani aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Ndipo moto wochokera kwa Yehova unabwera nʼkunyeketsa anthu 250 amene ankapereka nsembe yofukiza aja.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 16:35
14 Mawu Ofanana  

Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto; lawi lake lidapsereza oipawo.


Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.


Ndipo panatuluka moto pamaso pa Yehova, nuwatha, nafa iwo pamaso ya Yehova.


amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova.


nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.


ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.


Ndipo Aisraele onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kufuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.


ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro.


Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.


Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa