Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 24:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Zidzukulu za Aroni ndi izi. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 24:1
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.


ndi cha magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi cha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi cha zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;


Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.


mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa,


Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo.


Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Yehova.


Ndipo ansembe anatuluka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao;


Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.


Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.


mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu.


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.


Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara anabadwira Aroni.


Ndipo maina ao a ana aamuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.


Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa