Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.
Numeri 27:16 - Buku Lopatulika Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Inu Chauta, mwini mpweya wopatsa moyo anthu onse, musankhe munthu kuti aziyang'anira mpingowu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngati nʼkotheka Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, sankhani munthu woti ayangʼanire gulu ili kuti |
Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.
Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m'manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye.
fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.
ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.
Ndipo mfumu Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao.
Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita.
Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?
Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.
Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
Chifukwa chake siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.