Numeri 26:62 - Buku Lopatulika Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onse amene adaŵerengedwa mwa Aleviwo anali 23,000, kuyambira ana aamuna a mwezi umodzi ndi opitirirapo. Iwowo sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, chifukwa sadapatsidwe choloŵa pakati pa Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo. |
Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.
Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake aamuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.
owerengedwawo ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu mphambu makumi asanu ndi atatu.
Chifukwa chake Levi alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi abale ake; Yehova mwini wake ndiye cholowa chake, monga Yehova Mulungu wake ananena naye.
Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.
Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao.
Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko la hafu, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao.