Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:47 - Buku Lopatulika

47 Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Alevi okha sadaŵaŵerengere kumodzi ndi enawo, potsata banja la makolo ao,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:47
12 Mawu Ofanana  

Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.


Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse mu Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.


Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti,


koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.


Koma sanawerenge Alevi mwa ana a Israele; monga Yehova adauza Mose.


Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, nati


Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu.


Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa