Numeri 26:63 - Buku Lopatulika63 Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201463 Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa63 Ameneŵa ndiwo anthu amene adaŵerengedwa ndi Mose ndi wansembe Eleazara. Iwowo adaŵerenga Aisraelewo ku zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.