Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:64 - Buku Lopatulika

64 Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

64 Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

64 Koma pakati pa anthu ameneŵa panalibe ndi mmodzi yemwe wamoyo amene adaaŵerengedwa kale ndi Mose ndi wansembe Aroni, pamene ankaŵerenga Aisraelewo ku chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai;

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:64
10 Mawu Ofanana  

mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, monga mwa kuwerenga kwani konse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine;


Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno.


Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.


Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.


Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwere nao; pakuti anamwazika m'chipululu.


Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?


Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka mu Ejipito, anthu aamuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka mu Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa