Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:65 - Buku Lopatulika

65 Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

65 Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

65 Paja za iwowo Chauta adati, “Adzafera m'chipululu.” Sadatsale ndi mmodzi yemwe mwa iwo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:65
20 Mawu Ofanana  

Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana.


Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati,


Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno.


Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo.


Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.


Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.


Maina a amunawo ndiwo: wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune.


Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.


Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.


Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka mu Ejipito, anthu aamuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka mu Ejipito.


Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa