Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 14:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko la hafu, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko logawika pakati, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mose adagaŵira mafuko aŵiri ndi theka aja magawo ao a dziko kuvuma kwa Yordani, koma Alevi okha sadaŵagaŵire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mose anapereka kwa mafuko awiri ndi theka dziko la kummawa kwa Yorodani, koma fuko la Levi lokha silinagawiridwe malo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 14:3
9 Mawu Ofanana  

Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake.


Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi hafu la fuko la Manase, likhale cholowa chao.


Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.


Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba;


Hesiboni ndi mizinda yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni;


Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa