Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
Numeri 26:22 - Buku Lopatulika Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa, anthu okwanira 76,500, ndiwo anali a m'mabanja a Yuda, amene adaŵerengedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500. |
Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana aamuna a atate wako adzakuweramira.
Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);
Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.
Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.