Numeri 25:3 - Buku Lopatulika Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Aisraele adapembedza nao Baala wa ku Peori, ndipo Chauta adaŵapsera mtima Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motero Aisraeli anapembedza nawo Baala-Peori ndipo Yehova anawapsera mtima kwambiri. |
Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.
Sindidzalanga ana anu aakazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.
Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.
Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.
Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.
Kodi mphulupulu ya ku Peori itichipera, imene sitinadziyeretsere mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova,
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;