Hoseya 4:14 - Buku Lopatulika14 Sindidzalanga ana anu aakazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Sindidzalanga ana anu akazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi chifukwa chochita zachiwerewere, sindidzaŵalanga akamwana anu chifukwa cha zigololo zao. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo. Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 “Ine sindidzalanga ana anu aakazi pamene iwo adzachita zachiwerewere, kapena akazi a ana anu pamene adzachita zigololo. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako. Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu! Onani mutuwo |