Hoseya 4:13 - Buku Lopatulika13 Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu aakazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu akazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Amapereka nsembe pa mapiri, amafukiza lubani pa zitunda, patsinde pa mitengo yogudira monga thundu, mnjale ndi mkundi, chifukwa amati mithunzi yake njabwino. “Nchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere, ndipo akamwana anu akuchita zigololo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri ndi kufukiza lubani pa zitunda, pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi, pamene pali mthunzi wabwino. Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo. Onani mutuwo |