Yeremiya 17:4 - Buku Lopatulika4 Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Mudzataya dziko limene ndidakupatsani kuti likhale ngati choloŵa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithu mkwiyo wanga uli ngati moto woyaka, ndipo udzayakadi mpaka muyaya.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mudzataya dziko limene ndinakupatsani kuti likhale cholowa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu mʼdziko limene inu simukulidziwa, chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto, ndipo udzayaka mpaka muyaya.” Onani mutuwo |