Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake.
Numeri 24:3 - Buku Lopatulika Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Mau a Balamu mwana wa Beori, mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo ananena uthenga wake: “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka, |
Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake.
Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;
anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.
wakumva mau a Mulungu anenetsa, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.