Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 24:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 ndipo ananena uthenga wake: “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 ndipo adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Mau a Balamu mwana wa Beori, mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:3
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo Mikaya anayankha kuti, “Ndinaona Aisraeli onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mwamtendere.’ ”


Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.


Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:


Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake.


Pamenepo Balaamu ananena uthenga wake: “Nyamuka Balaki ndipo tamvera; Undimvere iwe mwana wa Zipori.


Ndipo Balaamu ananena uthenga wake: “Balaki ananditenga kuchoka ku Aramu, mfumu ya ku Mowabu kuchokera ku mapiri a kummawa. Iye anati, ‘Bwera, temberera Yakobo mʼmalo mwanga, pita nyoza Israeli.’


Ndipo iye ananena uthenga wake nati, “Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori, uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka.


Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, amene ali ndi nzeru zochokera kwa Wammwambamwamba, amene amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, amene amagwa chafufumimba koma diso lake lili lotsekuka:


uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa