Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:4 - Buku Lopatulika

4 wakumva mau a Mulungu anenetsa, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 anenetsa wakumva mau a Mulungu, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 munthu amene akumva mau a Mulungu, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ali chipenyere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu, yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse, yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:4
20 Mawu Ofanana  

Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.


Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.


Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake.


Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu.


Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.


Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;


Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo; zokhalamo zako, Israele!


koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka;


Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.


Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,


Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,


Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,


Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa