Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.
Numeri 23:12 - Buku Lopatulika Ndipo anayankha nati, Chimene achiika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ichi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayankha nati, Chimene achiika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ichi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adayankha kuti, “Kodi sindiyenera kulankhula zokhazo zimene Chauta adaika m'kamwa mwanga?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Kodi sindinayenera kuyankhula zimene Yehova anandiwuza?” |
Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite.
Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.
Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.
Kapena kulankhula, osachitsimikiza? Taonani, ndalandira mau akudalitsa, popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha.
Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?
Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.
Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.