Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 24:13 - Buku Lopatulika

13 Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 ‘Ngakhale Balaki andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindidzatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta wandiwuza. Sindidzachita zabwino kapena zoipa mwa kufuna kwanga. Ndidzalankhula zimene Chauta adzandiwuze?’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena?

Onani mutuwo Koperani




Numeri 24:13
6 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.


Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.


Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwangamwanga.


Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.


Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.


Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa