Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 23:26 - Buku Lopatulika

26 Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Koma Balamu adafunsa Balakiyo kuti, “Kodi sindidakuuzeni kuti ndiyenera kuchita zonse zimene Chauta wandiwuza?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 “Balaamu anayankha Balaki kuti, ‘Kodi sindinakuwuzeni kuti ndiyenera kuchita zimene Yehova wanena?’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:26
12 Mawu Ofanana  

Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.


Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.


Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.


Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova?


Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse.


Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.


Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera.


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa