Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 23:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Balaki adauza Balamu kuti, “Tiyeni limodzi tipite ku malo ena. Mwina mwake zidzamkondwetsa Mulungu kuti muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Kenaka Balaki anati kwa Balaamu, “Bwera ndikutengere ku malo ena. Mwina chidzamukondweretsa Mulungu kuti uwatemberere kumeneko mʼmalo mwanga.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:27
12 Mawu Ofanana  

Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita.


Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?


Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.


Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.


Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.


Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita?


Ndipo Balaki ananka naye Balamu pamwamba pa Peori, popenyana ndi chipululu.


Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa