Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza thumba ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.
Numeri 22:31 - Buku Lopatulika Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo Chauta adatsekula maso a Balamu, ndipo adaona mngelo wa Chauta ataimirira m'njira, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono Balamu adazyolika, nadziponya pansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake. |
Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza thumba ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.
Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.
anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso.
wakumva mau a Mulungu anenetsa, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka.
Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.
Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?
Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake?