Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.
Numeri 20:10 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m'thanthwe umu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m'thanthwe umu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose ndi Aroni adasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi kuthanthweko nauza anthuwo kuti, “Imvani anthu opandukanu. Kodi tichite kukutulutsirani madzi m'thanthwemu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose ndi Aaroni anasonkhanitsa anthuwo pamodzi ku thanthwelo ndipo Mose anawawuza kuti, “Tamverani osamvera inu, kodi tikupatseni madzi kuchokera ku thanthwe ili?” |
Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe mu Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele.
Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.