Numeri 2:12 - Buku Lopatulika Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiele mwana wa Zurishadai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiele mwana wa Zurishadai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Simeoni, limene mtsogoleri wake ndi Selumiele mwana wa Zurishadai, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Fuko la Simeoni lidzamanga pafupi ndi Rubeni. Mtsogoleri wa gulu la Simeoni ndi Selumieli mwana wa Zurisadai. |
Ndi khamu lake, ndi olembedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.
Ndi khamu lake ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Selumiele mwana wa Zurishadai.