Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 18:4 - Buku Lopatulika

Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa chihema chokomanako, kuchita ntchito yonse ya chihema; koma mlendo asayandikize inu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa chihema chokomanako, kuchita ntchito yonse ya chihema; koma mlendo asayandikize inu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iwo adzagwira nawe ntchito, ndi kumatumikiranso m'chihema chamsonkhano pa ntchito zonse zam'chihemamo. Ndipo wina aliyense asadzafike pafupi ndi inu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Azikhala ndi inu ndipo azisamalira ntchito yonse ya mu tenti ya msonkhano koma munthu wina aliyense wapadera sayenera kufika pafupi nanu.

Onani mutuwo



Numeri 18:4
10 Mawu Ofanana  

Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa Kachisi kwa utumiki wake wonse, ndi zonse zakumachitika m'mwemo.


Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa chihema chonse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.


Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele.


Koma uike Aroni ndi ana ake aamuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.


Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.


koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.


Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.